Cholinga chikuru cha Webusayiti iyi ya Nsenga Language Community nchakulongozhya njira yachangu na yachitukuko yakufikila Malemba Oyera mu chinenero cha chinsenga. Ichi chikulongoza kukula kwa uzimu na kulimbika kwa chikhulupiriro cha anthu onse okaamba chinsenga.
Kupanga Malemba Oyera mu chinenero chachibadwidwe, Webusayiti iyi yafuna kuti okamba chinsenga amvwishe bwino Mau a Mulungu, kuti masambilo a m’Baibolo akhale amoyo, omwe angamvwikeshe na kusintha mitima.
Pulatifomu iyi yakusonkhanitsa zinthu za pa dijito   kuphatikizhyapo mavidiyo, ma odio, na Baibolo yolembedwa  kuti anthu onse, akulu, na ana kumo, amene sadziwa kuwerenga, athe kumvwishya Mau a Mulungu. Imalimbikitsa kugwirizanitsa okhulupirira, abusa, na atsogoleri a mipingo, kuti apereke zinthu zakusambiza, kulalika, na chisamaliro mu chinsenga.
Pa chikhalidwe, Webusayiti iyi ikulimbikishya kusunga na kutukula chinenero na chikhalidwe cha chinsenga pogwiritsa ntchito Malemba Oyera. Polimbikishya kugwiritsa ntchito chinenero chachibadwidwe mu kulambira na kusambila, chimalimbikishya kuzindikira chiyambi na umunthu wa anthu a chinsenga.
Kupitishya ntchito iyi, Webusayiti ya Nsenga Language Community ikuwona tsogolo la anthu onse okamba chinsenga kuti akhale ndi mwayi wakukumana na Mau a Mulungu mu chinenero chimene chimalowa mu mtima, kuti atukuke mu chikhulupiriro cholimba na mgwilizano wamphamvu pakati pa Akhrisitu.

Bible Society of Zambia Membership Registration

Your encouragement is valuable to us

Your stories help make websites like this possible.